Yesu ndi ndani?

Analoseredwa ndi:

Daniel.

Ndinawona m’masompheya a usiku, taonani, anadza ndi mitambo ya kumwamba wina ngati mwana wa munthu, nafika kwa nkhalamba ya kale lomwe; ndipo anamyandikizitsa pamaso pake. Ndipo anampatsa ulamuliro, ndi ulemelero, ndi ufumu, kuti anthu onse, ndi mitundu yonse ya  anthu, ndi manenedwe onse, amtumikire; Ulamuliro wake ndi ulamuliro wosatha umene sudzachotsedwa, ndi ufumu wake sudzawonongeka.  Daniel 7:13-14

Yesaya.

Pakuti kwa ife mwana wakhanda wababwa, Kwa ife mwana wamwamuna wapatsidwa; ndipo ulamuliro udzakhala pa phewa lake, ndipo adzamutcha  dzina lake Wodabwitsa, Wauphungu, Mulungu wamphamvu, Atate wosatha, Kalonga wamtendere. Za kuyenjezera ulamuliro wake, ndi za mtendere sizidzatha pa mpando wachifumu wa Davide, ndi pa ufumu wake, kuwukhazikitsa, ndi kuwuchirikiza ndi chiweruzo ndi chilungamo kuyambira tsopano ndi kunkabe nthawi zosatha. Changu cha Yehova wa makamu chidzachita zimenezi.  Yesaya 9:6-7

Ndipo zonsezi zinakhala kuti chikachitike chonenedwa ndi Ambuye mwa mneneri, ndikuti "Onani namwali adzaima, Nadzabala mwana wamwamuna, ndipo adzamutcha dzina lake, EMANUELI; kuthandauuzira kwake, "MULUNGU NAFE."  Mateyu 1:22-23

Analambiridwa ndi:

Anzeru a kummawa.

Ndipo Iwo, m’mene anamva Kwa Mfumu ananyamuka; ndipo onani, nyenyezi ija anayiwona kum’mawa inawatsogolera Iwo, kufikira inadza niima pamwamba pomwe panali kamwanako. Ndipo iwo powona nyenyeziyo, anakondwera ndichikondwelero chachikulu. Ndipo pofika kunyumba anawona Mwanayo ndi Maria amayi ake, ndipo anagwa pansi namgwadira iye; namasula chuma chawo, nampatsa iye mphatso, ndiye Golidi ndi Libano ndi Mure.  Mateyu 2:9-11

Ophunzira ake.

Ndipo Pomwepo Yesu anatansa dzanja lake, nam’gwira iye, nanena naye, iwe wokhulupilira pang’ono, wakayikiranji mtima? Ndipo pamene iwo analowa m’ngalawamo, mphepo inaleka. Ndipo iwo amene anali m’ngalawamo anamgwadira nanena    "Zoonadi, ndinu Mwana wa Mulungu." Mateyu 14:31-33

Ndipo ophunzira ake Khumi ndi m’modzi anamuka ku Galileya, kuphiri kumene Yesu anawakonzera iwo. Ndipo pamene anamuwona Iye, anamlambira.  Mateyu 28:16-17

Ndipo anatuluka nawo kufikira ku Betaniya; nakweza manja Ake, nawadalitsa. Ndipo kunali, pakuwadalitsa Iye analekana nawo, natengedwa kunka kumwamba. Ndipo anamlambira Iye, nabwera ku Yerusalemu ndi chimwemwe chachikulu; ndipo anakhala chikhalire m’kachisi, nayamika Mulungu. Amen.  Luka 24:50-53

Amai anamuona akumpachika pamtanda.

Ndipo iwo anachoka msanga kumanda,ndi mantha ndikukondwera kwakukuru,nathamanga kukawuza ophunzira ake. Ndipo onani, Yesu anakomana nawo, nanena, Tikuwoneni. Ndipo iwo anadza, namgwiraIye mapazi ake, namgwadira. Pomwepo Yesu ananena kwa iwo “Musaope.” Mateyu 28:8-10

Wolemba ndi:

Adani a Yesu.

Koma Yesu anawayankha iwo, Atate wanga amagwira ntchito kufikira tsopano, Inenso ndigwira ntchito. Chifukwa cha ichi a Yuda anawonjeza kufuna kumupha. Sichifukwa cha kuswa Sabata kokha, komatu kuti amadzichanso kuti Mulungu ndi Atate Ake; nadziyerekeza wofanana ndi Mulungu.  Yohane 5:17-18

Ayuda anamyankha Iye, "Tili nalo lamulo ife, ndipo monga mwalamulo ayenera kufa, chifukwa anadziyerekeza kukhala Mwana wa Mulungu." Yohane 19:7

Mtumwi Petulo.

Yesu anawafunsa yiwo. "Inu mumati kuti ine ndine yani. Ndipo Simoni Petulo anayankha nati, "Inu ndinu Khristu, Mwana wa Mulungu wamoyo. Ndipo Yesu anamyankha iye nati, "Ndiwe wodala, Simoni Bar-Yona: pakuti thupi ndi mwazi sizinakuululire ichi, koma Atate wanga wakumwamba.”  Mateyu 16:15-17

Mtumwi Tomasi.

Yesu anadza, makomo ali chitsekere, nayimilira pakati pawo, nati, "Mtendere ukhale ndi Inu!"  Pomwepo ananena kwa Tomasi, "Bwera nacho chala chako kuno, nuone manja anga; ndipo bwera nalo dzanja lako, nuliike kunthiti yanga, ndipo usakhale wosakhulupilira." Tomasi anayankha nati kwa Iye, "Ambuye wanga ndi Mulungu wanga!" Yesu ananena kwa iye, "Chifukwa wandiona Ine, wakhulupilira: odala iwo akukhulupilira angakhale sanawone." Yohane 20:26-29

Yesu Mwini.

Ndipo onse anati, "kodi ndinu Mwana wa Mulungu?" Ndipo Iye anati Kwa Iwo, "Mwatero ndinu amene."  Luka 22:70

“Ine ndi Atate wanga ndife amodzi.” Yohane 10:30

“Iye amene waona Ine waonanso Atate Wanga.” Yohane 14:9




Nkhani zotsatirazi zikutifotokozera choonadi cha Uthenga wa Baibulo

1. DALAIVALA WAGALIMOTO

Tsiku lina Dalaivala woyendetsa Galimoto anayimitsidwa ndi apolosi apanseu. Anali wodziwa bwino ntchito yake ndipo ngakhale amayimitsidwa amadziwa kuti sanalakwe kalikonse.

Wapolisiyo anati “ndakuyimitsani chifukwa mumathamanga kwambiri pa mtunda wokwana makumi asanu ndi khumi pawola pamalo amene pali sukulu.Panali zikwangwani khumi zomwe zimakuchenjezani kuti mukuyenera kuyenda pang’ono pamtunda wokwana khumi ndi mphambu zisanu pawola.”

Monga momwe woyendetsa galimoto anali ndi zikwangwani khumi zomuchenjeza, Ifenso Mulungu anatipatsa zikwangwani zotichenjeza M’bukhu loyera. Amatchedwa Malamulo khumi.

Kodi munanamako, kuba kapena kulumbira pogwiritsa ntchito dzina la Mulungu? Ngati mudachitako ngati ine yankho lanu likuyenera kukhala “Inde”.

Mvetserani, Mau a Mulungu akuti:

Pakuti amene aliyense angasunge Malamulo onse, koma akakhumudwa palimodzi, iye wachimwira onse.  Yakobo  2:10

Mulungu akuti ngati tingaphwanye limodzi mwa Malamulo Khumi tachimwa ndipo tidzayankha Mlandu wopwanya wonse kuphatikiza dama ndi kuba.

Chiweruzo cha Mulungu pa Machimo athu ndi imfa. (Kuponyedwa Kugahena wamoto chifukwa sadzalora uchimo popezeka iye). Aroma 6:23a

Ngati nkhaniyi ingathere apa, ndiye kuti kulibe chiyembekezo cha Moyo wathu…


2. WOZENGEDWA MLANDU

Munthu wina wosalakwa anadza Kwa oweruza Milandu nadzipereka kuti aphedwe m’malo mwa chigawenga chomwe chinapezeka ndi mlandu wakupha ndipo anamubvomera. Tsiku lina Woweruza anawuza wakuphayo kuti akuyenera kupanga chisankho.

“Munthu wosalakwa wanyongedwa m’malo mwako. Ngati ungabvomereze kuti imfa yake yawombola mlandu wako uli womasuka kupita kwanu Mumtendere. Kapena ngati siubvomera udzanyongedwa ndithu pakuti unapalamula Mulandu. Usankhapo chiyani?”

Yesu Khristu, Mwana wa Mulungu analibe tchimo koma anapereka Moyo wake pakutifera pamtanda kuwombola ife tonse. (Chiweruzo cha Mulungu pa Moyo wathu wauchimo ndi imfa). Patatha Masiku atatu iye anauka Kwa akufa.

Koma Mulungu atsimikiza Kwa Ife chikondi chake cha mwini yekha m’menemo, kuti pakukhala Ife chikhalire ochimwa, Khristu anatifera ife.  Aroma 5: 8

Koma mphatso yaulere ya Mulungu ndiyo Moyo wosatha ya mwa Khristu yesu Ambuye Wathu. Aroma 6: 23b

Zotsatira zaimfa ya yesu pa mtanda m’malo mwathu, muli ndi zisankho ziwiri zoti muchite:

Kulandira Mamasulidwe amachimo anu ndi Moyo wasatha pakulapa machimo. (Kubvomereza machimo anu ndikupanga chisankho chowasiya ndikutembenukira Kwa Mulungu). Ndikuyika Chikhulupiliro chanu Kwa Ambuye Yesu.

Kapena;

Kukana Mamasulidwe auchimo ndi Moyo wosatha pokhulupilira Munthu Kapena Chilichonse Kuposera Ambuye Yesu amene angakupangitseni kukhala obvomerezeka Kwa Mulungu ndikulandira chilango chophwanya Malamulo a Mulungu.

Iye amene akhulupilira Mwanayo ali nawo Moyo wosatha; Koma iye amene sakhulupilira Mwanayo sadzaona Moyo, Koma mkwiyo wa Mulungu ukhala pa iye.  Yohane 3:36

Kudziwapo za Ambuye Yesu sizitanthauza kuti ndinu okhulupilira…


3. AKATSWIRI ODUMPHA MNDEGE

Akatswiri odumpha M’ndege amaonetsera chikhulupiliro chawo muzobvala zimene amabvala akamadumpha kuchokera mundege yili m’malere (parachuti).

Onse otsatira Ambuye Yesu amaonetsera chikhulupiliro chawo pa Iye pamene Mzimu wa Mulungu uwasintha m’malingaliro ndi muzikhumbo-khumbo zawo.

Chifukwa chache ngati munthu Ali yense Ali mwa Khristu Ali wolengedwa watsopano, zinthu zakale zapita, taonani zakhala zatsopano. 2 Akorinto 5:17.

Ndipo ndidzakupatsani Mtima watsopano, ndikulonga mkati mwanu Mzimu watsopano ndipo ndidzachotsa mtima wamwala mthupi, ndi kukupatsani Mtima wamnofu.  Ezikiel 36:26.

Ngati Kulowa m’malo amene amakonzerako magalimoto akawonongeka sizikupangitsani inu kukhala Mekaniki, choncho kupita kutchalitchi kokha sikungakupangitseni kukhala Mkhristu.

Ngati mungafune kupulumutsidwa ku machimo anu ndikupeza Moyo wosatha, Tsatirani pemphero motere:

“Ambuye Yesu, ndikukhulupilira kuti munandiwombola ku machimo anga pamene munafera pamtanda ndi kuuka kwa akufa. Ndikufuna kusiya moyo wanga wauchimo ndikuyika chikhulupiliro changa kwa inu ngati Ambuye ndi Mpulumutsi wanga. Ndakonzeka kuyenda nanu Masiku onse a Moyo wanga. Zikomo Ambuye pondipatsa Mphatso ya Moyo wosatha. Amen. ”

Pakuti aliyense adzaitanira padzina la Ambuye adzapulumuka.   Aroma 10:13

Kuti mukayende koyenera ambuye kukamkondweretsa monsemo, ndikubala zipatso muntchito yonse yabwino, ndikukula mzizindikiro cha Mulungu.  Akolose 1:10.